Chisamalilo pa nthawi imene mlandu wothetsa banja wayambika. Mwamuna kapena mkazi amene wayambitsa mlandu othetsa banja kapena ofuna kuti alekane kwa ka nthawi ali ndi ufulu opempha bwalo la milandu kuti lilamule mwamuna kapena mkazi kuti adzipeleka chisamalilo chosiyanasiyana kwa mkaziyo kapena mwamunayo pa nthawi imene akudikila kuti mlanduwo uthe. Chisamalilochi chimatchulidwa kuti “Chisamalilo choyembekezela kuweluza mlandu” ndipo chimathandiza mwamuna kapena mkazi kuti adzilandilabe chisamalilo kuchokera kwa mkazi wake kapena mwamuna wake angakhale ukwati wawo wasokonekera kapenapamene m’modzi mwa iwo wakadandaula ku bwalo la milandu. Izi zili chomwchi pozindikila kuti milandu imatenga nthawi kuti ithe kuzengedwa ndipo mwamuna kapena mkazi akuyenelabe kusamalidwa mpakana pamene bwalo lamilandu laweluza mlandu.Polamula mwamuna kapena mkazi kuti adzipeleka chisamalilo choyembekezela kuweluza mlandu, bwalo la milandu limawunika chuma chimene mwamuna ndi mkazi ali nacho komanso mfundo zina zimene bwalo lamilandu lingathe kulingalila. Chisamalilochi chimayenela kupelekedwa mpakana pamene bwalo la milandu lagamula kuti ukwati watha.